Saturday, October 26, 2013

TISAIWALE ZIFUKWA ZOMWE AMALAWI SITIDZAVOTERA PEOPLES PARTY MU CHISANKHO CHA 2014.


TISAIWALE


(This is just apart of an audio documentary which is available for free, you can request your copy by emailing magedesiwandale@gmail.com )

Mongokumbutsana:
  1. Peoples Party  siyikuikila kumtima pa chitetezo cha ife a Malawi pomwe mtchitidwe wa uchifwamba,kuba  komanso kuphana  zafika poyipa moti  ngakhale a president athu alibe chitetezo Kamba koti adaliuza dziko kuti iwo akumaospezedwa kuti aphedwa  kusonyeza kuti chitetezo mudziko muno mulibe tsono ngati presidenti wathu alibe chitetezo ife a Malawi ndife otetezedwa?

  1. Peoples Party yatengapo gawo  lalikulu pakubedwa kwa ndalama ku likulu la dziko lino kudzera mwa akuluakulu a chipani chawo monga a Osward Lutepo  pomwe masukulu ndi zipatala zikusowa ndalama ife a Malawi mkumavutika.


  1. Peoples Party  ikutinamiza kuti mudziko muno muli chakudya pomwe tikapita ku ADMARC tikumabwelako chabe chifukwa chakuti chimanga kulibe ife mkumagona ndi njala zomwe zikusonyeza kuti anthu awa samatiganizila ife a Malawi.

  1. Peoples Party  idanamiza mtundu wa a Malawi ndi  achinyamata kuti apita Ku South Korea kukagwira ntchito pomwe izi zinali zabodza pofuna kutipusitsa ife a Malawi kuti tikopeke nawo zomwe zidaonongetsanso ndalama zaboma pachabe .


  1. Peoples Party  idaoletsa chimanga  chambiri kunkhokwe za dziko la  Malawi munthawi yomwe  amalawi  tinkavutika ndi njala koma mpaka lero komwe chimanga chowolachi chidakatayidwa ngati dziko ife sitidziwa.

  1. Peoples Party ikunyalanyaza kutsegula  sukulu monga ya  Chancellor college,Polytechnic,College of Medicine komanso masukulu ena a ntchito zaunamwino Kamba kosowa ndalama zokozera zofuna aphunzitsi  ndi zofooka zina kupangitsa ife makolo komanso ana athu kukhala odandaula chifukwa tsogolo lawo silikuoneka pomwe iwo ali kalikiliki kuba ndalama za boma.


  1. Peoples Party yasonyeza kuti iwo saganizira ife a Malawi maka osauka chifukwa mu nthawi yomwe adagula magalimoto oyendera nduna ndi mabwana aku ESCOM ndi nthawi yomwe a Malawi timasowa mankhwala muzipatala komanso ma dotolo kumagwilitsa ntchito zida zomwe masiku ake ogwilitsila ntchito adatha chomwe ndichiopsezo kumiyoyo yathu kuonjezera apo,kutseka kwa malo ena ogwilira ntchito ya opaleshoni komanso kungozi ngati a Kamuzu Central Hospital komwe ife aMalawi osaukitsitsa timapezako thandizo.

  1. Peoples Party mu ndondomeko ya fetereza wamakuponi ya chaka cha 2012/2013 idatigulitsa ife a Malawi mchenga mmalo mwa feteleza zomwe zidapangitsa amalawi ena kuluza ndalama komanso kusapindula ndi ndondomekoyi,kuonjezela apo,mundondomeko ya chaka cha 2013/2014,amalawi ena omwe timapindula ndi ndondomekoyi atichotsamo chomwe chili ngati chipongwe kwa ife polingalira kuti ife ndife anthu osaukitsitsa omwe sitingathe kugula feteleza pa mtengo wa 15,000 kwacha.


A malawi anzanga, ine simunthu  Wandale ayi, iyi ndi mbali ya pologalamu yanga (Documentary) yofuna kuti ife amalawi tisanamizidwe ndi anthu andale koma tidziwe zowona zenizeni ndikupanga chisankho chabwino chosankha  mtsogoleri odzalamula  dziko lino mu chaka cha 2014.


By: Magede Si Wandale

No comments:

Post a Comment